Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.
Masalimo 50:2 - Buku Lopatulika Mulungu awalira mu Ziyoni, mokongola mwangwiro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu awalira m'Ziyoni, mokongola mwangwiro. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu akuŵala atakhala m'Ziyoni, mzinda wake wokongola kotheratu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri Mulungu akuwala. |
Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.
Anapenya mayendedwe anu, Mulungu, mayendedwe a Mulungu wanga, mfumu yanga, m'malo oyera.
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Dzanja lanu likhale pa munthu wa padzanja lamanja lanu; pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.
Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase, ndipo mutidzere kutipulumutsa.
M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana aakazi inu a ku Yerusalemu.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala padziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.
Onse opita panjira akuombera manja: Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati, kodi uwu ndi mzinda wotchedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?
Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.
Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.
Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.
Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala paphiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.
Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.
Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.