Masalimo 5:12 - Buku Lopatulika Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama; mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango. |
M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.
Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.