Masalimo 49:9 - Buku Lopatulika Kuti akhale ndi moyo osafa, osaona chivundi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kuti akhale ndi moyo osafa, osaona chivundi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti azikhalabe ndi moyo mpaka muyaya osapita ku manda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya ndi kusapita ku manda. |
Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.
Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa? Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?
Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udyo sudzapulumutsa akuzolowerana nao.
kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa mu Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.
Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,
iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwe m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaone chivunde.