Dani adzakhala njoka m'khwalala, songo panjira, imene iluma zitendene za kavalo, kuti womkwera wake agwe chambuyo.
Masalimo 49:5 - Buku Lopatulika Ndidzaoperanji masiku oipa, pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzaoperanji masiku oipa, pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndichitirenji mantha pa nthaŵi yamavuto pamene anthu ondizunza akundizinga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika, pamene achinyengo oyipa andizungulira. |
Dani adzakhala njoka m'khwalala, songo panjira, imene iluma zitendene za kavalo, kuti womkwera wake agwe chambuyo.
Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.
Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.
nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.
osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;
Chifukwa chake tsono, mwazi wanga usagwe pansi kutali ndi Yehova; pakuti mfumu ya Israele yatuluka kudzafuna nsabwe, monga munthu wosaka nkhwali pamapiri.