Masalimo 49:4 - Buku Lopatulika Ndidzatchera khutu kufanizo, ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzatchera khutu kufanizo, ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakupherani mwambi, ndidzamasulira tanthauzo lake poimba pangwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzatchera khutu langa ku mwambo, ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga. |
Ndipo potsiriza pake pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi.
Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.
kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.
Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati chidzalalikidwa pa matsindwi a nyumba.