Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
Masalimo 49:2 - Buku Lopatulika awamba ndi omveka omwe, achuma ndi aumphawi omwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 awamba ndi omveka omwe, achuma ndi aumphawi omwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa anthu otsika ndi okwera omwe, olemera ndi osauka omwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika, olemera pamodzinso ndi osauka: |
Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.
Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko ndi zinthu zonse zotulukamo.
Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye mu Kachisi wake wopatulika.