Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse.
Masalimo 49:16 - Buku Lopatulika Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usavutike munthu wina akamalemera, pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera, pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira; |
Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse.
Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.
Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.
Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.
Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.
Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.