Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 49:13 - Buku Lopatulika

Njira yao ino ndiyo kupusa kwao, koma akudza m'mbuyo avomereza mau ao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Njira yao yino ndiyo kupusa kwao, koma akudza m'mbuyo avomereza mau ao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zimenezi ndizo zimene zimaŵagwera anthu amene ali ndi chikhulupiriro chopusa, ndiwo mathero ake a onse amene amatsata maganizo otere.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha, ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula. Sela

Onani mutuwo



Masalimo 49:13
6 Mawu Ofanana  

Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe.


Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.


Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?


Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;