Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mzinda, nautcha dzina lake la mzindawo monga dzina la mwana wake, Enoki.
Masalimo 49:12 - Buku Lopatulika Koma munthu wa ulemu wake sakhalitsa, afanana ndi nyama zakuthengo, afanana nazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma munthu wa ulemu wake sakhalitsa, afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale munthu akhale wolemera chotani, komabe adzafa chabe ngati nyama zakuthengo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale munthu akhale wachuma chotani, adzafa ngati nyama. |
Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mzinda, nautcha dzina lake la mzindawo monga dzina la mwana wake, Enoki.
Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.
Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.
Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;