Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi abulu ao, misasa ili chimangire; nathawa apulumutse moyo wao.
Masalimo 48:6 - Buku Lopatulika Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira; anamva chowawa, ngati wam'chikuta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira; anamva chowawa, ngati wam'chikuta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adanjenjemera koopsa, ndipo adamva ululu wonga wa mkazi wovutika pa nthaŵi yochira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera, ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira. |
Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi abulu ao, misasa ili chimangire; nathawa apulumutse moyo wao.
Chifukwa chake m'chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona.
Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.
Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asachedwe mobalira ana.