Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
Masalimo 48:4 - Buku Lopatulika Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana, anapitira pamodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana, anapitira pamodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mafumu adasonkhana, adafuna kuuthira nkhondo pamodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene mafumu anasonkhana pamodzi, pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe, |
Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.
Tsiku limenelo adzaimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tili ndi mzinda wolimba; Iye adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga.
Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupambana.
Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure: