Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.
Masalimo 48:11 - Buku Lopatulika Likondwere phiri la Ziyoni, asekere ana aakazi a Yuda, chifukwa cha maweruzo anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Likondwere phiri la Ziyoni, asekere ana akazi a Yuda, chifukwa cha maweruzo anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu okhala mu Ziyoni akondwe. A ku Yuda asangalale chifukwa cha kaweruzidwe kanu kolungama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Phiri la Ziyoni likukondwera, midzi ya Yuda ndi yosangalala chifukwa cha maweruzo anu. |
Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.
Ziyoni anamva nakondwera, nasekerera ana aakazi a Yuda; chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.
Wakuda ine, koma wokongola, ana aakazinu a ku Yerusalemu, ngati mahema a Kedara, ngati nsalu zotchinga za Solomoni.
Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala zakuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini.
Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala yakuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini.
M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana aakazi inu a ku Yerusalemu.
awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.
Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana aakazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.
Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.
Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.
Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.