Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.
Masalimo 47:6 - Buku Lopatulika Imbirani Mulungu, imbirani; imbirani mfumu yathu, imbirani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Imbirani Mulungu, imbirani; imbirani mfumu yathu, imbirani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando; imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando. |
Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.
Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.
Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.
Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.
Ndipo Miriyamu anawayankha, Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.
Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: