Masalimo 45:5 - Buku Lopatulika Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mivi yanu ndi yakuthwa, imalasa mitima ya adani. Mitundu ina ya anthu imagwa pansi pamaso panu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu, mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu. |
Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.
Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.
Mulungu amtulutsa mu Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.
Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?
Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.
Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.
Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha ophunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.