Masalimo 45:16 - Buku Lopatulika M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inutu zidzukulu zanu zidzaloŵa m'malo mwa makolo anu, mudzaŵasandutsa mafumu pa dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako; udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse. |
Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.
Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.