Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.
Masalimo 45:12 - Buku Lopatulika Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu a ku Tiro adzakukopa ndi mphatso, olemera kwambiri adzakunyengerera Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso, amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako. |
Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.
Chifukwa cha Kachisi wanu wa mu Yerusalemu mafumu adzabwera nacho chaufulu kukupatsani.
Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.
Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka, ndipenye nkhope yako, ndimve mau ako; pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.
Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.
Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.