Masalimo 44:9 - Buku Lopatulika Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa; ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa; ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe Inu mwatitaya, ndipo mwatitsitsa, simunapite nawo limodzi ankhondo athu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa; Inu simupitanso ndi ankhondo athu. |
Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?
Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;
koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.