Masalimo 44:8 - Buku Lopatulika Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse, ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse, ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Takhala tikunyadira mphamvu za Mulungu nthaŵi zonse, ndipo tidzakuthokozani mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse, ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya. |
kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.