Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 44:1 - Buku Lopatulika

Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Inu Mulungu, ife tidamva ndi makutu athu, makolo athu adatiwuza za ntchito zimene mudagwira pa masiku ao, masiku amakedzana.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.

Onani mutuwo



Masalimo 44:1
16 Mawu Ofanana  

Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.


Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.


Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.


Ndinaganizira masiku akale, zaka zakalekale.


Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.


Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina.


Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani?


Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe chatigwera ife bwanji chonsechi? Ndipo zili kuti zodabwitsa zake zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweze kodi Yehova kuchokera mu Ejipito? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midiyani.