Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.
Masalimo 43:1 - Buku Lopatulika Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, onetsani kuti ine ndine wosalakwa, munditchinjirize pa mlandu wanga kwa anthu osasamala za Mulungu. Mundipulumutse kwa anthu onyenga ndi opanda chilungamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu; ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza; mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa. |
Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.
Pakuti nkhondo inatanda padziko lonse, ndipo tsiku lomwelo nkhalango inaononga anthu akuposa amene anaonongeka ndi lupanga.
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.
Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu, Yehova Mulungu wanga; ndipo asandisekerere ine.
Mudzaononga iwo akunena bodza; munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.
Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.
Yehova aweruza anthu mlandu; mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa, ndi ungwiro wanga uli mwa ine.
Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.
Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa, m'dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa.
Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake.
Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.
amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;
Chifukwa chake Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, nandigwirire moyo, nandipulumutse m'dzanja lanu.