Mundikonzeranso mboni zonditsutsa, ndi kundichulukitsira mkwiyo wanu; nkhondo yobwerezabwereza yandigwera.
Masalimo 42:7 - Buku Lopatulika Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Madzi akuya akuitanizana ndi madzi akuyanso, mathithi anu akulindima kochititsa mantha. Mafunde anu ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe andimiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Madzi akuya akuyitana madzi akuya mu mkokomo wa mathithi anu; mafunde anu onse obwera mwamphamvu andimiza. |
Mundikonzeranso mboni zonditsutsa, ndi kundichulukitsira mkwiyo wanu; nkhondo yobwerezabwereza yandigwera.
Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m'kamphindi.
Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.
Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, ndipo madzi anandizinga; mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
Ndipo muja tinalanda dziko m'manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Heremoni;