Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.
Masalimo 41:13 - Buku Lopatulika Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli kuchokera muyaya mpaka muyaya. Ameni ndi Ameni. |
Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.
Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova.
Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.
Wodala Yehova, Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndi anthu onse anene, Amen. Aleluya.
Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am'nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno.
ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m'chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.
Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.
Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.
ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.