ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Masalimo 40:7 - Buku Lopatulika Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza; m'buku mwalembedwa za Ine, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza; m'buku mwalembedwa za Ine, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndidati, “Ndilipo, ndikubwera, monga zidalembedwa za ine m'buku la malamulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera. Mʼbuku mwalembedwa za ine. |
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu.
Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.
Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhale wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.
Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha.
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;
Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti onse akumkhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ao, mwa dzina lake.
Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.