Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Masalimo 40:2 - Buku Lopatulika Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko, mʼthope ndi mʼchithaphwi; Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba. |
Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.
Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.
Ndamira m'thope lozama, lopanda poponderapo; ndalowa m'madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza.
Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.
Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi, monga ndende zimasonkhanitsidwa m'dzenje, ndi kutsekeredwa m'kaidi, ndipo atapita masiku ambiri adzawazonda.
Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.
yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.