Masalimo 40:16 - Buku Lopatulika Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma iwo amene amafunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!” |
Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
Ozunzika adzadya nadzakhuta, adzayamika Yehova iwo amene amfuna, ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.
Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa, ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.
Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero.
Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Ha! Wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;
Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika.