Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova.
Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza.
Pulumutseni Yehova; Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.
Koma Inu, Yehova, musakhale kutali; mphamvu yanga Inu, mufulumire kundithandiza.
Fulumirani kundithandiza, Ambuye, chipulumutso changa.
Mabala anga anunkha, adaola, chifukwa cha kupusa kwanga.
Musandikhalire kutali, Mulungu; fulumirani kundithandiza, Mulungu.