Ndipo iye anati kwa abale ake, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, zili kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzake kuti, Nchiyani ichi Mulungu watichitira ife?
Masalimo 40:12 - Buku Lopatulika Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira; machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona. Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga, ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga. |
Ndipo iye anati kwa abale ake, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, zili kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzake kuti, Nchiyani ichi Mulungu watichitira ife?
Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.
Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.
Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.
anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.
Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.
Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;