Masalimo 40:1 - Buku Lopatulika Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga. |
Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.
Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mzinda udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka.