Masalimo 39:8 - Buku Lopatulika Ndipulumutseni kwa zolakwa zanga zonse, musandiike ndikhale chotonza cha wopusa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipulumutseni kwa zolakwa zanga zonse, musandiike ndikhale chotonza cha wopusa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse. Musandisandutse chinthu chochinyodola zitsiru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse; musandisandutse chonyozeka kwa opusa. |
Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.
Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.
Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.
Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.
Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?
Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ake, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale chitonzo mwa amitundu;
Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.