Ha? Mukadandibisa kumanda, mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.
Masalimo 39:4 - Buku Lopatulika Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa, ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati; ndidziwe malekezero anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa, ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati; ndidziwe malekezero anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Inu Chauta, mundidziŵitse mathero a moyo wanga, mundidziŵitse kuchepa kwa masiku anga. Mundilangize kuti moyo wanga sukhalira kutha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga ndi chiwerengero cha masiku anga; mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani. |
Ha? Mukadandibisa kumanda, mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.