Masalimo 39:2 - Buku Lopatulika Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala chete osalawa chokoma; ndipo chisoni changa chinabuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala chete osalawa chokoma; ndipo chisoni changa chinabuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero ndidakhala chete osalankhula kanthu, ndidakhala duu, koma popanda phindu, chifukwa mavuto anga ankangokulirakulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pamene ndinali chete osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino mavuto anga anachulukirabe. |
Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.