Masalimo 39:11 - Buku Lopatulika Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mumalanga munthu pakumdzudzula chifukwa cha uchimo wake. Mumaonongeratu zimene iye amazikonda, monga m'mene chimachitira chifukufuku. Zoonadi, munthu aliyense ndi mpweya chabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo; mumawononga chuma chawo monga njenjete; munthu aliyense ali ngati mpweya. Sela |
kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi, amene kuzika kwao kuli m'fumbi, angothudzulidwa ngati njenjete.
Taonani, Ambuye Yehova adzathandiza Ine; ndani amene adzanditsutsa? Taonani, iwo onse adzatha ngati chovala, njenjete zidzawadya.
kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.
koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo.
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.