Masalimo 39:10 - Buku Lopatulika Mundichotsere chovutitsa chanu; pandithera ine chifukwa cha kulanga kwa dzanja lanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundichotsere chovutitsa chanu; pandithera ine chifukwa cha kulanga kwa dzanja lanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Chotsani chikoti chanu pa ine, ndatheratu chifukwa cha mkwapulo wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chotsani mkwapulo wanu pa ine; ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu. |
Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.
Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi? Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?
Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.
Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.