Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;
Masalimo 38:9 - Buku Lopatulika Ambuye, chikhumbo changa chonse chili pamaso panu; ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ambuye, chikhumbo changa chonse chili pamaso panu; ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ambuye, mumadziŵa zonse zimene ndimakhumba, kusisima kwanga sikuli kosamveka kwa Inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye, kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu. |
Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;
Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.
Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.
Pakutinso m'menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba;