ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamutu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira mu Mwamba.
Masalimo 38:5 - Buku Lopatulika Mabala anga anunkha, adaola, chifukwa cha kupusa kwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mabala anga anunkha, adaola, chifukwa cha kupusa kwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mabala anga aola ndipo akununkha chifukwa cha kupusa kwanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mabala anga akuwola ndipo akununkha chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo. |
ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamutu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira mu Mwamba.
Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.
Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?