Masalimo 38:12 - Buku Lopatulika Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ofunafuna moyo wanga, amanditchera misampha. Ofuna kundipweteka amalankhula zondiwononga, tsiku lonse amangolingalira zondichita chiwembu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo, oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga; tsiku lonse amakonza zachinyengo. |
Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake.
Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.
Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.
Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya; ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.
Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.
Abale onse a wosauka amuda; nanga mabwenzi ake kodi satanimphirana naye? Awatsata ndi mau, koma kuli zii.