Masalimo 38:10 - Buku Lopatulika Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yachoka, ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandichokera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yachoka, ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandichokera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtima wanga ukugunda, mphamvu zandithera, ndipo sindikutha kupenya bwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha; ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga. |
Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwaa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.
Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.
Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira.
Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.