Masalimo 38:1 - Buku Lopatulika Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu, ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu, ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta musandikwiyire ndi kundidzudzula. Musapse mtima ndi kundilanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova musandidzudzule mutapsa mtima kapena kundilanga muli ndi ukali. |
Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.
M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako.
Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula.
Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.
Pakuti ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukali, umene Yehova anakwiya nao pa inu kukuonongani. Koma Yehova anandimvera nthawi ijanso.