Masalimo 37:2 - Buku Lopatulika Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pakuti monga udzu iwo adzafota msanga, ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga. |
chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha.
Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;