Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 37:1 - Buku Lopatulika

Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;

Onani mutuwo



Masalimo 37:1
12 Mawu Ofanana  

Anthu oongoka mtima adzadabwa nacho, ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsutsa wonyoza Mulunguyo.


Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.


Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.


Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; mtima wake udandaula pa Yehova.


Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse.


Usachitire nsanje anthu oipa, ngakhale kufuna kukhala nao;


Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa; ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu.


Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse.


koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.


njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.