ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.
Masalimo 34:4 - Buku Lopatulika Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha; anandilanditsa ku mantha anga onse. |
ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.
M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.
Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.
Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.
Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa, ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.
Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.
Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,
Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.