Masalimo 33:9 - Buku Lopatulika Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pakuti Iye adalankhula, ndipo zidachitikadi, adalamula, ndipo zidaonekadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo; Iye analamulira ndipo zinakhazikika. |
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Mboni zanu zivomerezeka ndithu; chiyero chiyenera nyumba yanu, Yehova, kunthawi za muyaya.
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,
Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwe kuchokera mu zoonekazo.
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.