M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
Masalimo 33:1 - Buku Lopatulika Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima, oongoka mtima ayenera kulemekeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima, oongoka mtima ayenera kulemekeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kondwerani mwa Chauta, inu anthu ake. Zoonadi ochita zolungama azitamanda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama, nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo. |
M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.
Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.
Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.
Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.