Masalimo 30:7 - Buku Lopatulika Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu; munabisa nkhope yanu; ndinaopa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu; munabisa nkhope yanu; ndinaopa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa cha kukoma mtima kwanu, Inu Chauta, mudandikhazikitsa ngati phiri lolimba. Koma pamene mudandimana madalitso anu, ine ndidataya mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima. |
Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao.
Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.
Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,
Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao; ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.
Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.
Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?