Masalimo 30:6 - Buku Lopatulika Ndipo ine, ndinanena m'phindu langa, sindidzagwedezeka nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ine, ndinanena m'phindu langa, sindidzagwedezeka nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ine, pamene zinthu zidaandiyendera bwino, ndidati, “Sindidzagwedezeka konse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, “Sindidzagwedezekanso.” |
Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.
Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalire izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake.
Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta chakumwa chaukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikulu loposa ndithu.
Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?
Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.
Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.