Masalimo 30:3 - Buku Lopatulika Yehova munabweza moyo wanga kumanda, munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova munabweza moyo wanga kumanda, munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, mwanditulutsa m'dziko la akufa, mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje. |
Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa, simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe? Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu m'kuunika kwa amoyo.
Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.
Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
Ambuye ndi zinthu izi anthu akhala ndi moyo. Ndipo m'menemo monse muli moyo wa mzimu wanga; Chifukwa chake mundichiritse ine, ndi kundikhalitsa ndi moyo.