Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana.
Masalimo 30:2 - Buku Lopatulika Yehova, Mulungu wanga, ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, Mulungu wanga, ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta, Mulungu wanga, ndidalirira Inu kuti mundithandize, ndipo mwandichiritsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa. |
Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana.
Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.
Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.
Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu, Yehova Mulungu wanga; ndipo asandisekerere ine.
Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.
Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.