Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.
Masalimo 30:12 - Buku Lopatulika kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya. |
Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.
ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wachisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.
Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo; inde, moyo wanga umene munaombola.
ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.