Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
Masalimo 30:10 - Buku Lopatulika Mverani, Yehova, ndipo ndichitireni chifundo, Yehova, mundithandize ndi Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mverani, Yehova, ndipo ndichitireni chifundo, Yehova, mundithandize ndi Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Imvani, Inu Chauta, ndipo mundikomere mtima. Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa.” |
Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.