Masalimo 28:1 - Buku Lopatulika Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikuitana Inu Chauta, Inu thanthwe langa, musachite ngati simukundimva, chifukwa ngati mukhala chete, ndidzafanafana ndi anthu otsikira ku manda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa; musakhale osamva kwa ine. Pakuti mukapitirira kukhala chete, ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje. |
Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje? Ngati fumbi lidzayamika Inu? Ngati lidzalalikira choonadi chanu?
Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.
Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?
Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera.
Chigumula chisandifotsere, ndipo chakuya chisandimize; ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje.
Ndidzafuulira kwa Mulungu ndi mau anga; kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzanditcherezera khutu.
Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.
Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni; Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.
namponya ku chiphompho chakuya, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthawi.